Apolisi ayamba kuchititsa maphunziro

Apolisi m’boma la Salima ati ayamba kuchita maphunziro a okhudza umoyo wa anthu, chisamaliro cha ana, chitetezo cha m’mudzi komanso malingaliro a ngwiro.
Inspector Rita Lazalo kuchokera ku nthambi yoona za chitetezo cha m’mudzi komanso kuthetsa nkhanza ati maphunzirowa akuchitika tsiku ndi tsiku kuti anthu akhale otetezeka komanso odziwa maufulu awo.
M’modzi mwa ophunzira, Group Village Headman Kili a ku Kuntimasonjo, ati aphunzira mmene angapewere maganizo odzichotsera moyo komanso kusamalira bwino mabanja awo.
Iwo atinso aphunzira kusamala pogawana uthenga kuti apewe kugwiritsidwa ntchito molakwika ndi anthu ena.
Iwo alonjeza kufalitsa uthengawu m’mudzi mwawo komanso apempha anthu kupewa nkhanza kwa ana aakazi monga kugwiririra chifukwa kumaphwanya ufulu wawo.
Wolemba Alice Lissa Kamwanje

About Us

Love Holdings Limited is an umbrella organization committed to bridging communication and action for development. We combine trusted community broadcasting with practical agricultural solutions to create measurable social and economic impact.

Salima, Malawi