Alonjeza Kupititsa Chitukuko Patsogolo

Ngati njira imodzi yolimbikitsa chipani cha DPP m’dera lapakati m’boma la salima, a Symon Vuwa Kaunda omwe adaimira chipanichi m’derali ngati phungu alonjeza kugwira ntchito ndiotsatira chipanichi pofuna kupititsa patsogolo chitukoko m’delari.
Poyankhula pa mkumano omwe anali nawo ndi otsatira chipanichi lachinayi, a Kaunda ati aika ndondomeko monga kutukura masewero, kuthandiza anthu m’midzi komanso kugwira ntchito ndi mabugwe osiyana siyana.
Ndipo m’mawu ake khansala wa Boma ward, George Josephy anati ndiokondwa ndi ndondomekozi ponena kiti zithandizira chipani cha DPP mu delari.
Akulu akulu ochokera kuma area osiyana siyana achipanichi anali nawo pa mkumanowu.
Wolemba Brighton Elisha.

About Us

Love Holdings Limited is an umbrella organization committed to bridging communication and action for development. We combine trusted community broadcasting with practical agricultural solutions to create measurable social and economic impact.

Salima, Malawi